Karonga Ayionetsa Bangwe
By Vinjeru Betera Mkandawire……
Timu ya Bangwe All Stars yochokera Mzinza wotchuka ndi malonda Blantyre yagonjetsa timu ya Karonga United pakhomo pawo ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi.
Timu ya Karonga inayamba bwino pomwe inapeza mipata ingapo koma goloboyi wa Bangwe Elias Missi anali tcheru kutchinjiriza golo lake zomwe zinapangitsa timu ya karonga isapeze chigoli chotsegulira masewera.
Ndipo panali pa 38 mimutes pomwe mnyamata Phillip Chavula anapereka mpira wabwino kwa mnyamata osewera kutsogolo Michael Tetteh yemwe anangosumbira kuti Bangwe itsogole ndipo chigawo choyamba chinathera momwemo.
Chigawo chachiwiri timu ya karonga inabwera ndi mtima ofuna kubweza chigoli koma anyamata awo akutsogola amangoohonya ndipo izi zinapangitsa mphunzitsi wa timuyi Kondwa Ikwanga kuchotsamo Sheriff Shamama, Alfred Chizinga komanso Allen Chihana nkulowetsa Saulos Moyo, Davie Tobias komanso Steve Saka.
Pa mphindi zokwana 72 mnyamata wa Bangwe Innocent Msowoya anakoka mpira kuchokera patali atalandira mpira kuchokera kwa Chikumbutso Salima kuti atsogoze timu ya Bangwe.
Chigoli chachiwiri chinazidzimutsa timu ya karonga ndipo inayamba kupanikiza zomwe zinapangitsa bangwe kusakhazikika mu golo lawo Mpakana mnyamata wawo anagwira malo olesedwa kupangitsa woimbira kulodza pa malo a imfa ndipo mnyamata Davie Tobias ndamene anagoletsa kuti ukhale 2 kwa 1.
Karonga inapitiliza kuopereka chiopsyezo Ku timu ya bangwe koma sizinaphule kathu pomwe woyimbira anayimba wenzulo kuti masewera athera momwemo 2 kwa 1 kukomera timu ya bangwe all stars.
Poyankhulapo atatha masewera Kondwa Ikwanga mphunzitsi wa Karonga anati anyamata ake aphonya kwambiri komanso kuvulala kwa osewera ake awiri kunawasokoneza.
“Chilango umalandira ndi chimenechi ukakhala kuti sukugwiritsa bwino mipata chifukwa tapeza mipata yambiri koma takanika kuchinya anzathu kungopeza yochepa agwiritsa nchito komanso kuvulara kwa Justin Banda ndi Sunganani Mponda kunatisokoneza kwambiri koma tibwelera pa ground kuti tikakonze momwe mwalakwika”. Anatero Ikwanga
Ndipo Nzake Mavuto Tiganna Lungu wati iye ndokondwa kupeza chipambano chake choyamba komanso kukhala koyenda.
” Ndine osangalala kwambiri ndi anyamata anga popeza chipambano koyenda sichophweka ndithu monga muziwa Ku Blantyre ndikutali komanso ndithokoze mwini timu komanso azitsogoleri onse a Bangwe potipatsa zonse timafuna zomwe zimapangitsa anyamata kuchilimika posewera mpira” Lungu anatero
Timu ya Karonga Sabata ikubwerayi izasewera ndi timu Civil Service United pamene Bangwe isewera ndi FCB Nyasa Big Bullets.
Masewera apakati pamatimu awiriwa ndalama zokwana 2.7 million kwacha zomwe zapedzeka pakhomo atamaliza kuwerengesera.
