2026-04-17

Hammer Rangers ya M’Boma la Lilongwe ikupempha Thandizo

0
IMG-20230410-WA0032

Wolemba: Hosea Banda……

Pomwe ligi za mdziko muno Zikhale zikuyamba mwezi wa April, zadziwika kuti kusoweka Kwa thandizo azachuma ndi chithu chimodzi chomwe chikupangitsa kuti matimu ambiri ochokera m’madera akumidzi asamatenge nawo mbali mu maligi azigawo komanso maboma ambiri mdziko muno.

Izi zadziwika pomwe kafukufuku wa The Malawi Guardian online wapeza kuti timu ya Hammer Rangers yochokera Kwa Pondamali m’boma la Lilongwe ikukanika kutenga nawo mbali mu ligi ya Boma la Lilongwe kamba kosowekera thandizo la za chuma.

Mwini wake wa timuyi Francis Kalere wati timuyi imadalira kuchita maganyu ngati okolora chimanga minda yawanthu ngati njira imodzi yoti izithandizikira.

“Ngati njira imodzi yoti tizithandizikira, timachita maganyu okolora chimanga minda ya anthu osiyanasiyana ndipo ndalama zomwe timapeza sizikwanira kuti tingathe kutenga nawo mbali mu ligi ya Boma la Lilongwe komanso ya chigawo chapakati.”

Kalere wati akupepha anthu akufuna kwabwino omwe angathe kuwathandiza Ndi ndalama komanso mayendedwe kuti timuyi iyambe kutenga nawo mbali mu maligiwa.

“Thandizo lomwe tingafune kuti anthu akufuna kwabwino atithandize nalo Ndi monga ndalama komanso mayendedwe kuti timuyi iyambe kuyenda bwino ndikuyamba kutenga nawo mbali mu ligi ya Boma la Lilongwe.”

Mawu ake woyankhulapo pa nkhani za masewero Zachariah Kasakula wati pakufunika kuti akuluakulu oyendetsa masewero zigawo ayambe kuyendera matimu omwe Ali Madera akumidzi ndikuwathandiza mmene angapezere thandizo la zachuma lithandizira matimu awo.

“Pakufunika kuti akuluakulu oyendetsa masewero zigawo zonse za dziko lino ayambe kuyendera matimu onse omwe Ali Madera akumidzi ndikuwafikila ndikuwathandiza ndi upangiri wamomwe angapezere owathandiza kuti ayambe nawo kutenga mbali mu maligi azigawo komanso pa Boma.”

Iye wati matimu ambiri akukanika kutenga nawo mbali kamba kakuti sangakwanitse kulipira ndalima yomwe imalipiridwa ngati timu ikufuna kutenga nawo mbali mu ligi komanso mayendedwe.

Timu ya Hammer Rangers inayamba mchaka ch 2008 ndipo kufikila pano sinayambe watenga nawo mbali mu ligi ya chigawo chapakati komanso ligi ya Boma la Lilongwe.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *