St Gabriel yayamba zokonzekera zake

Wolemba: Hosea Banda…….
Mphunzitsi wa timu yamiyendo ya St Gabriel medicals Coach Mthetho Martin Kamanga wati ayambapo zokozekera za mchaka Cha Mpira cha 2023 lachiwiri pa 21 February 2023.
Polankhula Ndi The Malawi Guardian online iye wati zokezekerazi ayamba Ndi osewera kale komanso atsopano ngati njira imodzi yolimbitsira timuyi.
Mphunzitsitu anawonjezera kunena kuti mpaka pano sadziwa chifukwa chomwe timu yawo inachitseredwera ma poyitsi asanu Ndi imodzi(6) komanso chifukwa chomwe timuyi sinapitilire mundime ya matimu asanu Ndi imodzi (Round of 6) mu ligi ya chigawo chapakati ya Chipiku premier Division.
“Pa matimu omwe anapitirira mu ndime ya matimu khumi asanu Ndi imodzi ifeyo ngati ST Gabriel medicals tinachotseredwa mapoyitsi asanu Ndi imodzi (6) ndipo pomwe amatichotsera ma poyitsi asanu Ndi imodzi tinali pa nambala yoyamba.
Zifukwa zomwe anatichotsera mapoyitsiwa amazidziwa Ndi a Central Region Football Association (CRFA) ndizomwe zinatipangitsa kuti tisapitilire mu ndime ya matimu asanu Ndi imodzi (6)”.
Timu ya ST Gabriel medicals inakwanitsa kutenga ukatswiri wa chikho Cha Nyasa Capital finance ya chigawo chapakati.

