2026-04-16

Rwanda Paul Kagame Wasankha Mwana Wake Wamkazi Ngati Mlangizi Wa Pulezidenti

0
IMG-20230803-WA0014

Mtsogoleli wa dziko la Rwanda Paul Kagame wasankha mwana wake pa udindo mu boma lake.

Ange Kagame yemwe ndi wa zaka 29 amusankha kukhala wachiwiri kwa mkulu oyendetsa khonsolo yoona momwe ndondomeko za boma zosiyanasiyana zikugwilira ntchito.

Ange Kagame wakhala akugwira kale ntchito mu ofesi ya bambo ake kuyambira chaka cha 2019 ngati wamkulu oyang’anira ndondomeko zomwe ofesi ya mtsogoleli wa dzikolo zikugwirira ntchito zake.

Kusankhidwa kwa Ange kwaonjera chiwelengero cha ana a Kagame omwe anapatsidwa ntchito m’boma la bambo awo kufika pa atatu tsopano.

Mwana wa a Paul Kagame wamkulu ,Ivan Kagame ali mu bodi yoona zachitukuko cha dzikolo ndipo analowa pa udindo mu 2020.

Mwana wina Ian ali nawo mu gulu la a chitetezo a mtsogoleli wa dzikolo.

Credit: Nkhoma Fm

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *