Bungwe la Dzuka Malawi Lapempha Adindo a Chipani Cha UDF kuti Akasankhe Mwanzeru ku Koniveshoni
Bungwe lomwe limafunila zabwino chipani Cha United Democratic Front UDF lotchedwa Dzuka Malawi Lapempha adindo omwe Ali ndi kuthekela kukakhala nawo mtsonkhano waukulu wa Chipanichi kuti akakhale ndi masomphenya posankha adindo omwe Ali ndikuthekela kukwanilisa maloto a dziko lino.
Poyankhula Kwa atolankhani lachisanu mu Mzinda wa Mzuzu, Mlembi wamkulu wa bungweli a Evelyn Chitungu wati iwo akupempha ma delegeti kuti akasankhe wolemekezeka Atupele Muluzi.

“Posachedwapa Chipani chathu chokondedwa Cha UDF chikhala chikupita ku Convention, ku Convention imeneyo monga ife a UDF amene tinabwelesa demokalase mdziko muno timuwonesesa kuti, anthu akasankhe mwa ufulu mopanda kukakamizidwa, komanso chipani chilole wina Aliyense kukapikisan nawo pa mpando ulionse womwe iye akufuna, kuwonjezela apo Aliyense wopikisana nawo akavomeleze zosatila za chisankho chimenechi,”.
A Chitungu anawonjezela kuti ngati bungwe akupeleka sapoti pambuyo pa Atupele Muluzi.
“Akulu akulu a Bungweli titachimva kuti Wolemekezeka Atupele Muluzi asiya ndale ndipo asiyanso udindo ngati mtsogoleli wa chipanichi sitinachimve bwino ndipo tinaganiza zokhazikisa gululi ndicholinga tiwafikile a Bwana Atupele Muluzi kuti asinthe maganizo awo, ndipo tinapita kukakumana nawo ndikuwalimbikisa kuti abwelele kupanga ndale komanso kuti akapikisane nawo pa mpando wa mtsogoleli wa chipanichi ku Koniveshoni ndikuti azapikisane nawo pa chisankho Cha dziko mu Chaka Cha 2025,”
“Kuyambila pamenepo Dzuka Malawi yakhala ikupeleka sapoti yochuluka Kwa Atupele Muluzi pochitisa misonkhano madela osiyana siyana mu dziko lino monga Salima,Dedza, Zomba, Machinga, Blantyre ndi Zomba. Pameneponso ngati ife a Dzuka Malawi takhala tikusatila misonkhano madela osiyana siyana a chipani Cha United Democratic Front UDF,” anatele a Evelyn Chitungu.

Poyankhulapo Wamkulu wa Chipani Cha UDF chigawo chakumpoto(Viphya Region) Mayi Logester Msofi anati Iwo ndiwokondwa chifukwa Cha mtsonkhanowo kamba ka kuti unali wopindilila ambiri.
“Ndine wokondwa mtsiku la lero, mtsonkhano unali wabwino ndipo ngati Chipani tikuyenela kumva maganizo ambali zonse pomwe tikupita ku Koniveshoni ku Blantyre pa 2 October, 2024,”
Iwo anawonjezela kuti ngati chigawo Cha Viphya region agwilizana kukasankha Atupele Muluzi.
“Ngati Chipani tilibe maganizo olowa mu mgwilizano ndi zipani Zina, ndipo ngati chigawo Cha Viphya tagwilizana kuti tikasankhe Baambo Atupele Muluzi ngati mtsogoleli wa chipanichi ndipo kuti azatiyimilile pa chisankho Cha Dziko Chaka chamawa,” amatelo Mayi Msofi.

Mtsonkhano uyu kumabwelanso wachiwiri kwa Mkulu wabungweli Bambo Dickson Chidindo, Mayi Karim amene ndi wachiwiri kwa Mkulu wa amayi mu bungweli, Ibrahim Swank wachiwiri kwa msumhi chuma ndi akulu akulu ena a Bungweli.

Bungwe la Dzuka Malawi mosogozedwa ndi wapambando wawo Banbo Saifullah Kongwe ndi bungwe lomwe muli anthu ochokela madela osiyana siyana.u dziko la Malawi muzigawo zakumwela, Pakati, ku mpoto komanso ku chigawo chakuzambwe komanso mayilo ena amu Africa,
