Ntchito za Manja Zipereka Danga kwa Anthu Aulumali mu Mzinda wa Lilongwe
By Samson Kanyimbo……....
Pamene anthu aulumali wosiyanasiya achitenga kupepha ngati njira imodzi yopezera zosowa zawo m’matauni ndi m’mizinda ya dziko muno, Philemon Thomas akusimba lokoma ndi luso losoka nsapato.
Philemon ndi mnyamata wa zaka 25 zakubadwa yemwe ali ndi ulumali wosamva komanso kuyakhula m’mudzi mwa a Thomas mfumu yaikulu Tsabango, mzinda wa Lilongwe. Iye anati anachiona cha nzeru kuphunzira kusoka nsapato ngati njira imodzi yopezera zosowa za moyo wake kusiyana ndikumapephapepha.
Philemon anafotokozera The Malawi Guardian online kuti atamaliza maphunziro ake aku sekondale anachiona chinthu cha nzeru kuphunzira kusoka nsapato kusiyana ndikumadikilira kuti alembedwe ntchito Kapena kumapita mumisewu ndi matauni kumakapepha chinthandizo.
Philemon anati amafunitsitsa atazatsekula kampani yokoza nsapato ndikulemba ntchito anthu aluso losiyanasiyana komamso aulumali wosiyanasiyana.
M’modzi mwa anthu omwe amazasoketsa nsapato zake pamalo omwe Philemon amagwilirapo ntchito zake zosoka nsapato ndipo anati ndizosowa kuona munthu waulumali atayika chidwi pa ntchito za manja ngati kusoka nsapato, kuotchelera zinthu zosiyanasiyana ndi zina zambiri.
Polankhula Ndi The Malawi Guardian online m’modzi mwa ophunzitsa kubungwe loyang’anira anthu aulumali la Malawi Council for the Handicapped (MACOHA), a Alexander sinoya wati akanakonda boma litachitapo kathu pamaphunziro antchito za manja ndi zaluso komanso anthu aulumali wosiyanasiya chifukwa izi zithandiza anthu aulumali kuzidalira komanso kuziimira paokha.
A Siyano anati kupatula kuizimira paokha anthu aulumali athanso kumalembana ntchito okhaokha. Komamso boma litha kupulumutsa ndalama zomwe limapereka kumabungwe omwe amayakang’anira ndi kuthandiza anthu aulumali ngati anthuwa akutha kuziimira paokha kudzera ku ntchito za manja zomwe anaphunzitsidwa.
Follow Us on Twitte: @GuardianMalawi1
