Palibe chomwe chinalakwika pa masewero a Bullets ndi Silver, yatero FAM
Bungwe la zamasewero a miyendo mdziko muno la football association of Malawi (FAM) kudzera kuthambi yake yowona oyimbira mpira ya Football Association of Malawi Referees Committee yati oyimbira Mwayi Msungama sadakwitse kalikonse pa masewero a FCB Nyasa Big Bullets ndi Silver strikers.
Malingana ndi kalata yomwe bungweli latulutsa yati oyimbira Mwayi Msungama sanalakwitse popereka penate ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets komanso kusalora chigoli Cha silver strikers popeza kuti izi zinachitika kamba kakuti oyimbirayu anatsata malamulo a masewerowa.
“Kutsatira dandaulo lomwe timu ya silver strikers linasuma powonetsa kusakondwa ndi kukaniridwa chigoli komanso kupatsidwa penate bungwe lathu lapeza kuti oyimbira anatsata malamulo popaga ziganizo zonsezi.”
Kalatayi yapitiriza kunena kuti bungweli lipitiliza kuonetsetsa kuti chilungamo chikuchitika ku masewero onse a mpira mdziko muno.
Timu ya silver strikers inakasuma ku bungwe la FAM posakondwa ndi ziganizo zomwe oyimbira mpira Mwayi Msungama anachita pa masewero awo amu TNM super league ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets omwe inagonja ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi ponena kuti oyimbirayu anakana chigoli chawo komanso anapereka penate ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets.
Masewerowa anachitika pa 5 October 2025 pa bwalo la kamuzu stadium ndipo Hassan Kajoke ndi Ephraim Kondowe angoletsera timu ya Bullets pomwe Andrew Josephy angoletsera timu ya silver strikers.
