Kanema yotchedwa “Sinister Bonds” yakhazikisidwa pa intaneti tsopano
Popitiliza kuthandiza achinyamata kudzera mu kuwalimbikitsa pa za luso maka za kupanga mafilimi gawo lachiwiri ya “Sinister Bonds” filimu yomwe Director Isaac wathandizira kutulutsa kudzera mu ophunzira a pa MCA tsopano yakhazikitsidwa pa internet kudzera pa IPLUS PLAY usiku wa pa 2 August 2024.
Malinga ndi Misoya ,gawo la filimuyi momwe muli atenga mbali monga m’modzi mwa oyimba nyimbo za uzimu wodziwika steve wazisomo Muliya, Benson,Oscar,Chantelle,komanso Smacks ikufotokoza bwino za mphamvu zina zomwe zimaononga achinyamata pa zikhalidwe zotengera kuchokera kwa anzawo malo monga msukulu makamaka zomwe zili za ukachenjede ndi sukulu ya MCA ndiwomwe ili ndi atenga mbali a filimuyi.
Iye wati gawo la filimuyi ukuonetsa zina mwa khalidwe losasamalira pokutailira ndipo filimuyi ikulimbikitsa kuganiza mozama ndi kupanga chisakho chabwino.
“Sinister Bonds” idzionetsefwa kudzera pa internet pa app ya IPLUS PlAY ndipo magawo ena idzapangidwa sabata lililonse ndipo mpaka onse adzakwana magaqo 13 pamapeto.Ndipo anthu adzipeza zambiri za magawo a filimuyi potsegura website ya http://iplusplay.com
