Gulu Lipempha Ken Zikhale Ng’oma, Charles Kalumo atule pansi maudindo awo
By Evance Matola……
Gulu lina la nzika zina zokhudzidwa lapempha mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera kuti afotokozere mtundu wa aMalawi nthawi yeniyeni yomwe anthu ayambirenso kupangitsa zitupa zoyendera (passport) ku nthambi ya immigration.
Wapampando wa gululi Edward Kambanje wakumbusanso nduna yoona chitetezo cha mdziko Dr Kenneth Zikhale Ng’oma komanso mkulu wa nthambi ya immigration aCharles Kalumo kuti atule pansi maudindo awo popeza alephera ntchito yawo.
Kambanje wati ndizokhumudwitsa kuti ndunayi inanamiza dziko ponena kuti boma lagula makina atsopano omwe azipanga ziphaso zokwana 3000 pa tsiku .
Apa gululi lalengeza kuti lichita m’bindikiro ku maofesi aboma ku capital hill munzinda wa Lilongwe komanso ku maofesi a immigration pa 8 May 2024 pofuna kuti madando awo amveke.
Posachedwapa Dr Ken Zikhale Ng’oma adayendera likulu la nthambi yoona zolowa ndi zotuluka ku Blantyre komwe adaonetsa kukhumudwa ndi chidodo pa ntchito yopanga passport.
Pakadali pano mbali ya boma sinalankhulepo kanthu pa nkhawa za nzika zokhudzidwazi.
