2026-04-17

Engineer Vitumbiko Mumba Wakanidwa

0
Screenshot_20240806-111052~2

Engineer Vitumbiko Mumba yemwe anaonetsa chidwi chopikisana nawo pa udindo wa wachiwirinkwa mtsogoleli ku chipani cha Malawi Congress (MCP) sapikisana nawo kaamba koti dzina lawo palibe pa mndandanda wa anthu opikisana pa udindowu.

Mayina a anthu omwe avomelezedwa pa udindowu ndi a Catherine Gotani Hara,a Moses Kunkuyu,a Ken Zikhale Ng’oma komanso a Kezzie Msukwa.

Izi zaziwika pomwe Wapampando wakomiti yomwe ikuyendetsa msonkhanowu a Kezzie Msukwa atalengeza mayina a anthu omwe awavomeleza kukayima ku komveshoniyi pamsonkhano wa atolankhani omwe ukuchitikira mu mzinda wa Lilongwe.

A Simplex Chithyola Banda, a Richard Chimwendo Banda, a Eisenhower Mkaka, a Chris Chaima Banda, a Dyson Kamphambe ndi Dr. Albert Mbawala ndiwo omwe apikisane pa udindo wa mlembi wamkulu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *