Andipempha Kuti Ndikayime ku Nkhotakota
Katswiri woimba, Skeffa Chimoto wati aimira ngati phungu wa nyumba ya malamulo ku mdera la kummwera chakumvuma kwa boma la Nkhotakota pa chisankho cha chaka chamawa.
Chimoto wauza Mtolankhani wathu kuti ganizoli ladza anthu a delari atamupempha.
Iye wati akaimira chipani cha Malawi Congress Party ngati adzapambane pa chisankho cha chipulula cha chipani ku delari.
Watero Chimoto: “Pressure idachokera kumudzi kwathu komweko ndiye poyamba ndimakana koma nditalingalira ndidadzifunsa kuti bwanji anthu onsewa asankha ine?”
Chimoto ndi woyimba woziwika bwino mu mdziko muno.
