2026-04-16

Thandizeni ndili mu ululu woopsa, atero Mr Jefu

0
IMG-20241014-WA0005

Katswiri opanga thabwala pa masamba a mchezo yemwe amadziwika kuti ” Mr Jefu” ndipo dzina lake lenileni ndi Levinson Geoffrey Banda wapepha anthu akufuna mkwabwino kuti amuthandize ndi zithu zosiyanasiyana pomwe akudwala.

Polankhula ndi The Malawi Guardian Jefu wati iye akumvutitikila mayendedwe pomwe mwendo wake omwe ukungotuluka mafinya kamba chotupa chomwe chinamutuluka ndipo chinaphulika.

Iye wati mvutoli linamuyamba mchaka cha 2019 pomwe anali mdziko la Zambia mu komwe amakachita malonda pomwe anayamba kumva kuwawa mwendo wake wakumazere.

“Ndili mdziko la Zambia komwe ndimakachita malonga anga ndipomwe ndiyamba kumva kuwawa mwendo wanga wakumazere, ndipo ndinayesetsetsa kugula mankhwala koma palibe chomwe chinachitika chifukwa ululu unali ukukulabe.”

“Apa ndipomwe ndinaganiza zobwerera ku mudzi kwathu ku Mchinji.”

Jefu wati anayesera kupita ku chipatala chachikulu Cha Kamuzu Central kuti akalandile thandizo la mankhwala pa mvuto lomwe Ali nalo la mwendo koma palibe chomwe chinachitika.

Iye anati atafika pachipatala Cha Kamuzu Central anamufunsa kuti awapatse zikalata zochokera kuchipatala Cha Mchinji koma iye anati anabwera kuchipatalachi mwakufuna kwake ndipo achipatala anamuuza kuti mvuto lomwe ali nalo likufunika kuti apangidwe opaleshoni yomwe kufikira pano sinachitikebe.

“Ndinayesera kupita pa chipatala cha boma ku Mchinji koma amandipatsa mankhwala omwe ndimaona kuti sindimathandizika.

“Apa ndinalimgalira zopita ku chipatala chachikulu cha Kamuzu Central ku Lilongwe komwe andiuza kuti ndikufunika opaleshoni yomwe sinachitike mpaka lero.”

Jefu wawonjezera kunena kuti izi zamupangitsa kuti luso lake lopanga thabwala likhale lomvuta kamba kakuti akumvutikira mayendwe.

Iye wapepha anthu akufuna kwabwino kuti atha kumuthandiza ndi thandizo la ndalama kuti apite ku chipatala kukalandira thandizo la mvuto lomwe ali nalo la mwendo komanso thandizo la makina a kompiyuta (Computer) ndiso makina ojambulira zithuzo (Camera) kuti athe kupitiliza luso lake lojambula thabwala.

Iye wati onse amene akufuna kumuthandiza ndi thandizo lililonse atha kulumikizana naye pa nambala iyi +265994997723

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *