2026-04-16

Chilumba Cha Likoma sichili pa msika- yatero Nduna ya Zokopa alendo

0
IMG-20241009-WA0001

 

Nduna yokopa alendo a Vera Kamtukule yati phekesera zomwe zimamveka kuti chilumba cha Likoma chikugulitsidwa ndi abodza.

Ndunayi yanena izi pamkumano omwe unalipo pa khosolo ya Likoma omwe ndunayi inayitanitsa ndi adindo okhudzidwa apa chilumbachi ndipo inauza adindowa kuti zomwe zikumveka kuti chilumba cha Likoma chikugulitsidwa ndi zabodza.

“Ndaima pano kuti ndikutsimikizireni kuti malipoti omwe akumveka kuti boma likugulitsa chilumba Cha Likoma ndi abodza komanso palibepo tsiku lomwe boma linakhala pansi ndikukambirana zogulitsa chilumbachi komanso kusamutsa anthu ake kupita kumtunda.”

Kamtukule anawonjezera kunena kuti boma layika ndondomeko zabwino zofuna kupititsa patsongolo ntchito zachitukuko zokopa alendo (Tourism Master Plan) mdziko muno muzaka makumi awiri zikubwera (20-years) ndipo imodzi mwa ntchitozi ndizotukulira chilumba Cha Likoma.

“”Ntchito ndi monga Malo ofikilapo sitima komanso malo ogona alendo.”

Ndipo mawu ake mfumu yayikulu Mkumpha yachitatu (III) yayamikila nduna yokopa alendoyi kamba ka uthenga wawo wachimbikitso pa nkhani yokhudza chilumba Cha Likoma.

“Zomwe achita andunawa zachotsa matha omwe anthu anali nawo pa chilumba pano ndipo izi zasonyeza kuti boma lili ndi chikondi ndi anthu ake.”

Pa mkumanowu panali mafumu, makhasala komanso bwana mkubwa wa chilumba cha Likoma.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *