2026-04-16

Chidakwa Chinakana Ngongole ya Thobwa, Ife takana, nyimboyi siyathu, atero ma Blacks

0
FB_IMG_1728331520656

 

Gulu loyimba nyimbo la The Black Missionaries lati nyimbo yomwe ikuzungulira m’masamba a mchezo yonyoza mtsongoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera si yawo.

Malingana ndi uthenga omwe gululi latulutsa, lati yemwe wanjambula nyimboyi anayesera kufanizira mawu a yemwe amatsongolera gululi Anjiru Fumulani komanso kufanizira momwe gululi liyimbira nyimbo zake.

” Wojambula nyimboyi wayesera kufanizira mawu a mtsongoleri wathu Anjiru Fumulani komanso kufanizira momwe ife tiyimbira.” Yatero mbali imodzi ya uthengawu.

Gululi lati nalo ndi lodabwitsika kuti anthu ambiri omwe amatsatira gululi ayamba kutumiza nyimboyi kwa ena omwe ali mu gulu la The Black Missionaries kuti awawuze chilungamo ngati nyimboyi ayimba ndi iwo.

Ndipo gululi latsindika kunena kuti nyimbo yomwe anthu akugawanayi sanayimbe ndi Iwo.

Nyimbo yomwe anthu akugawanayi ndipo ikukamba monyoza mtsongoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera ikumati

“ndinaluza voti yanga pakuvotera mbava.”

“zithu zinakwera monga mwa dzina lako chakwera.”

Mbali Ina nyimboyi ikupiliza kunena zoyamikila atsongoleri akale a dziko la Malawi a Bakili Muluzi komanso a Peter Muntharika.

Ena mwa mawu omwe akunenedwa mu nyimboyi omwe ndi oyamikila a Bakili Muluzi ndi a Peter Muntharika monga awa:

“Tinazimenyera tokha ufulu ndipo tiyamike a chair ntchito munagwira.”

“Ndinanyoza Adadi ndi kuvotera mbavayi.”

Gulu la The Black Missionaries lati ilo ntchito yawo ndi kuyimba nyimbo zomwe ndi zobweretsa mtendere, chikondi komanso umodzi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *