2025-04-17

MABLEM ya yakhulapo pa khani ya chigamulo cha Bushili

0
IMG-20250320-WA0000~2

Bungwe lomenyera ufulu wa anthu la MABLEM, lachititsa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Lilongwe, kuyakhulapo pa chigamulo cha bwalo la milandu pa milandu yomwe a Shepherd Bushiri ndi a Mary akuyembekeka kukayankha mdziko la South Africa.

Bwalo la milandu linalamula kuti a Bushiri ndi akazi wawo awatumize mdziko la south africa kuti akayankhe milandu monga yogwilira komanso kudzembetsa ndalama.

Koma malinga ndi wapampando wa bodi ya bungwelo, a Robert Mkwezalamba ati
miyoyo ya anthuwa ili pachiophyezo ngakhale dziko lino silikuonetsa chidwi choteteza awiriwa, ponena kuti milanduyi ndiyochita kukonza.

A Mkwazalamba apempha dziko lino kuti liwonetsetse kuti a Bushiri komanso akazi awo atetezeka komanso lifunse dziko la South Africa kuti litsimikize za chitetezo chokhwima pa miyoyo ya anthu awiriwa, asanawatumize mdzikolo.

Iwo atsindikanso kuti ngati dziko la South Africa siliwonetsa chidwi pokhazikitsa ndondomeko zotetezera miyoyo ya awiriwa, dziko lino lisalole kuti awiriwa apite Ku South Africa.

Amatsogolela msonkhanowu ndi wapampando wabungweli Robert Mkwezalamba

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *