2025-03-19

MACRA yapempha mabungwe kuti athandize kuphuzitsa anthu za ufulu wa kungwilitsa tchito intaneti

0
IMG-20250313-WA0007

Bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) lapempha mabungwe m’dziko muno kuti alithandize kudziwitsa ndi kuphunzitsa anthu zokhudza ufulu wawo pomwe akugwiritsa ntchito intaneti.

Mkulu wa MACRA, a Daud Suleman, ayankhula izi ku Lilongwe komwe akuphunzitsa mabungwe osiyanasiyana ochokera mchigawo chapakati.

A Suleman afotokozeranso zamabilu atsopano omwe akuyembekezeka kupita kunyumba yamalamulo pokonzanso ndikukuza lamulo la mchaka cha 2016 kambaa koti zambiri zasintha muzaka zimenezi ndipo chiwerengero cha anthu ogwiritsa ntchito intaneti chikukwera tsiku ndi tsiku.

Iwo ati malamulowa ndi oti ateteze ana, amayi komanso anthu omwe amagwiritsa ntchito intaneti.

Mlangizi wa mtsogoleri wadziko lino pankhani za mabungwe omwe si aboma a Martha Kwataine alangiza anthu omamenyera ufulu wa anthu kuti adzionetsetsa kuti akufalitsa uthenga kapenanso nkhani zokhazo zimene zili zotsimikizika ndikulemekeza ufulu wa ena.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *