Mabungwe a MEC ndi NRB akupitilizabe ndi ntchito zawo molunjika zisankho-Mtalimanja

Bungwe loona ndi kuyendetsa zachisankho la MEC latsimikizira atolankhani kuti nkhani zonse za kalembera wa zisakho m’chakachi zipitilira kuyenda bwino pomwe ntchitoyi ikupitilirabe molingana ndi kulumikizana ndi ntchito zina za bungwe lopanga ziphaso la NRB.
Bungwe la MEC lalengeza kuti lichititsa kalembera wachisankho wachibwereza kuyambira pa 21 January mpaka 3 February.
M’mawo ake lachisanu lapitali mu mzinda wa Blantyre, wapampando wabungweli a Annabel Mtalimanja wati okhawo omwe analembetsa cha unzika kuyambira pa 21 October 2024 mpaka pa 4 January 2025 ndiwo akuloledwa kulembetsa.
Kalemberayu achitika mbali zina za madera ovotera okwana 1974 m’maboma onse kwa masiku awiri pa dera lililonse ndipo ntchitoyi itha sabata imodzi pomwe maderawa adzitsegulidwa m’mamawa 8 koloko ndikutsekedwa 4 koloko madzuro.
Anthu 271 sausande ndiwo akuyembekerezeka kulembetsa.