Achinyamata ndatsogololi apano yatelo nduna ya zachinyamata
Achinyamata ndatsogololi apano yatelo nduna ya zachinyamata
By Judgement katika
Nduna yowona za achinyamata ndi masewero a Uchizi Mkandawire yati lingaliro loti achinyamata ndiwo atsogoleri a masomphenya a chitukuko cha dziko lino linadza poona kuthekera komwe ali nako.
A Mkandawire alankhula izi lero ku Lilongwe pa msonkhano wa achinyamata wapa chaka omwe lakonza ndi bungwe la National Youth Council of Malawi (NYCOM).
Iwo ati kumbali yake utsogoleri wa dziko lino ukuonetsetsa kuti nthambi za boma zotukula achinyamata monga NYCOM zikupatsidwa thandizo la ndalama zokwanira kuti ntchito zawo zikafikire madera akumidzi.
Mkulu wa bungwe la NYCOM a Rex Chapota wati dziko lino lachedwa ndi ulendo otsogoza achinyamata pa chitukuko, ndipo wapempha mbali zokhudzidwa kuti zigwirane manja ndi magulu a achinyamata pokwanilitsa masomphenya a achitukuko aja a Malawi 2063.
Achinyamata oposa 500 kuchokera mmadera osiyanasiyana a dziko lino ndi omwe asonkhana ku Lilongwe pazokambiranazi komweso akhazikitsa ndondomeko ziwiri zachitukuko za achinyamata.