2025-03-18

UDF ikupitilirabe kupeza njira zolimbikitsa chipani pomwe tikuyandikira zisankho

0
IMG-20241029-WA0096

Chipani cha United Democratic Front(UDF) Chakhazikitsa komiti ina yomwe idziona za ubale wake ndi anthu otsatira chipanichi mwapadera pokumva maganizo awo ndi kuwalumikizitsa ndi komiti yaikulu ya National Executive Committee(NEC).

Poyankhula pamwambowu lolemba mu mzinda wa Blantyre, Mtsogoleri wa Chipanichi a Atupele Muluzi ati ganizoli ladza pofuna kupanga chipanichi kukhala chokomera anthu onse makanso pomwe tikuyandira zisankho za patatu mu m’chaka cha 2025.

“Tapanga izi ngati njira younikira zina zomwe anthu alinazo m’maganizo awo kuti tizimve ndi kuzigwilitsa ntchito pokonza zofooka zina mu chipanichi Kuti tikatenge boma tidzalamulire mokomera anthu onse” anatero a Muluzi.

Ndipo m’mawu ake,msungi chuma wamkulu wa chipanichi mai Yowoyani Greenwell anati kusiyana kwa ntchito za makomiti awiriwa ndikoti komiti yatsopanoyi(National Working Committee)idzipita mulunjika anthu omwe analibe mwayi weniweni opereka maganizo awo ku komiti yayikulu ya NEC ndikutenga maganizo awo kupita nawo ku kwa adindo akuluakulu onse a NEC.

Izi zikudza patangodutsa miyezi yochepa chabe pomwe chipanichi chinachititsa msonkhano wake waukulu wosankha adindo ake atsopano m’mipando yonse mu mzindawu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *