2024-11-04

Makwinja aAyamikila ma Kampani pothandiza Anthu mu Mzinda wa Blantyre

0

Mfumu ya mzinda wa Blantyre a Joseph Makwinja ati ndiokodwa ndi kampani zomwe zikuchita ntchito zawo zabwino pofuna kuphula anthu pa moto wa ena mwa mavuto omwe dziko lino likupitilira kukumana nawo.

Amakwinja alakhula izi loweruka pa mwambo wolimbikitsa nkhani za malonda monga a Galimoto,Njinga Zamoto mwa zina,ku makata mu mzindawu.

“Ndaona galimoto zoyendera magetsi,komanso mabank osiyanasiyana omwe abwera pano kuthandiza kuti anthu adzigula galimotozi polipila pang’ono pang’ono,

“izi zithandiza kuti anthu khaleko pa miwoyo yofewa ndi kupepukidwa pa za kusowa kwa mafuta ,komamso anthu ena apeza ntchito m’makapaniwa,ndine okondwera zedi,tiyeni tiike patsogolo ntchito zimenezi” anatero a Makwinji.

Ndipo m’mawu ake mmodzi mwa akuluakulu oyendetsa mwambowu omwe anautcha kuti Blantyre Motor Show, Alinane Njolomole anati sizinali zophweka kuti izi zitheke ndipo ndiwokondwa.

“Unali mtunda wolemetsa kuti izi zitheke motere ,ndife okondwa kuti anthu aonetsa chidwi chachikulu podzaonerera nawo zomwe zikuchitika ndipo tikukhulupilira kuti malonda a galimoto ndi njinga zamoto komanso mabank apita patsogolo”watero Njolomole.

Ena mwa makampani omwe anali nawo pa mwambowu ndi monga K.Motor, Adams Car Hire, Nissan, ndipo ndalama zankhanikhani zapelekedwa kudzera mu gwilizano wa makampani osiyanasiyana motsogozedwa ndi Lilongwe Motor Show Limited Komanso K.motors.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *