Gawo lomvetsera nyimbo usanatulutse chimbale ndilofunikira, watero DNA
Pomwe akukozekera kunkhazikitsa chimbale chake cha “Che Kaliwo” katswiri woyimba nyimbo DNA yemwe dzina lake lenileni ndi Daniel Kaliwo waloza mwambo omwe anthu akamvere nyimbo zake ndikupereka maganizo awo.
DNA wati wakoza mwambowu ndicholinga chakuti akamve maganizo a anthu osiyanasiyana pa nyimbo zomwe zili mu mchimbale cha Che Kaliwo chomwe chikhale akuchikhazikitsa posachedwapa.
“Gawo lomvetsera nyimbo limeneri ndi njira imodzi yomwe ndikufuna ndikamve maganizo a anthu pa ntchito yomwe ndagwira mu mchimbale cha Che Kaliwo.
“Maganizo amenewa ndikufuna kuti achokere kwa atolankhani, ojambula nyimbo ndi ma DJ kongonenapo ochepa chabe.”
Iye wati njirayi akafuna kuti aperekenso mpata kwa onse amane amatsatira nyimbo zake komanso omwe satsatira nyimbo zambo zake ngati mbali imodzi yolimbikitsa ubale wake ndi anthu osiyanasiyana.
DNA anawonjezera kunena kuti mwambowu ndi wawulere ndipo palibe wina aliyese yemwe akapise thumba Mwale ndikulira kuti akaonere mwambowu.
Iye wati wapanga izi polingalira mmene dziko likuyendera maka pa nkhani ya makina amakono a intaneti (internet) yomwe anthu amatha kupanga mkumanowu koma iye walingalira za anthu omwe sangakwanitse.
“Masiku ano ndi internet anthu ena amatha kungopita pa pasamba a mchezo a You Tube komanso Facebook ndikukhala ndi mwambo ngati umenewu mkumangoona mkupereka maganizo awo.
“Nditaona izi ndinazindikira kuti nditha kupereka mwayi kwa anthu enanso apadera kuti adzafike mkupereka maganizo awo pa chimbale chimenechi kwa onse ondidziwa komanso omwe sindidziwa, chifukwa chake sitikulipilitsa.”
Chimbale chimenechi chomwe chanyamula nyimbo nkhumi ndi zitatu (13) chili ndi uthenga umene watsamika pa nkhani zachikondi ngati kukhumudwitsa, kudana kulangizana, komanso kumvetsetsana muchikondi.
Chimbalechi ndi chachitatu kutsatira zimbale Zina ngati, Dziko la amuna komanso Mizizi.
Mwambowu omwe ukachitire ku MUHO Club ku chitipa boma la Lilongwe pa 26 October 2024 kukakhala oyimba ena ngati Taimon Tipa komanso katswiri ochokera mdziko la Zambia, Don Kingston zambia