2025-01-21

Dzuka Malawi Iyamikila Gavanala wa Chipani Cha UDF Chigawo Chakumpoto

0

 

Bungwe lotchedwa Dzuka Malawi lachisanu layamikila ndi kufunila mafuno abwino Mayi Logester Msofi pakusankhidwa kwawo ngati Gavanala wa Chipani Cha UDF chigawo chakumpoto (Viphya Region).

Chitungu Kupeleka mafuno abwino

Mawu awo Mlembi wamkulu wa bungweli a Evelyn Chitungu wati a Msofi ngati mmodzi wama membala a Dzuka Malawi akuyenela kupasidwa Ulemu kwambiri.

“Ife a Dzuka Malawi lero tabwera kuno ku chigawo chakumpoto kuzapeleka mafunso abwino Kwa mmodzi wama membala athu pakusankhidwa kwawo ngati Gavanala wa Chipani Cha UDF chigawo chakumpoto (Viphya Region).

Ife tingowafunila zabwino zonse pa mpando umenewu ndipo tikuwapemphanso kuti ngati mtsogoleli akuyenela kukonda ma membala onse achipanichi kusayang:anila mtundu kapena mdela komwe akuchokela,” anatelo a Chitungu.

Wachiwiri kwa msungi Chuma wa gula la DZUKA MALAWI yemwenso akuyimila ngati wachiwiri kwa mtsogoleli wa Chipani Cha UDF chigawo chakumpoto ku Koniveshoni Bambo Ibrahim Swank anati mayi Msofi ndi munthu yomwe amakonda Chipani Cha UDF.

“Mayiwa ndi munthu yemwe Ali wolimbika pa nkhani zandale ndipo ndili ndi chikhulupiliro kuti mpando wawo uthandiza kukweza Chipani Cha UDF kuno ku mpoto,”.

Poyankhula a Logester Msofi ayamikila akulu abungweli potenga nthawi yawo kuzawachezela ku ma ofesi awo.

“Ine kwanga ndikuyamika pa zomwe achita anthu awa, sichapafupi kupeza nthawi mpaka kuzandithikoza pakusankhidwa kwanga, Ambuye awadalise kothelatu,” Msofi.

Mwambowu inachitikila Kuma ofesi a chipani Cha UDF chigawo chakumpoto Mzinda wa Mzuzu.

Akulu akulu a Bungwe la DZUKA MALAWI komanso achipani Cha UDF anali nawo pa mwambowu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *