2024-10-11

Ntchito yotsitsa mafuta kuchoka musitima ilikati

0

 

Ntchito yotsitsa mafuta kuchokera mu Sitima yomwe yafika m’dziko lino dzulo ku Marka m’boma la Nsanje kuchokera ku Beira ili mkati padakali pano.

M’neneri wa bungwe loona za mafuta m’dziko lino, a Raymond Likambale, wati lero kuti galimoto zonyamula mafuta 17 zikuyembekezeka kunyamuka ku Nsanje kupita ku malo osungirako mafuta a Matindi munzinda wa Blantyre.

M’neneri wa bungwe lotolera misonkho m’dziko muno la Malawi Revenue Authority (MRA), a Steven Kapoloma, wati kulandira mafuta kudzera ku Marka Nyathando kuthandiza kuchepetsa kuchulukana kwa galimoto zonyamula mafuta zomwe zimayima mu zipata za dziko lino ku Songwe ndi Mwanza.

A Kapoloma atinso izi zithandiza kuti bungwe la MRA lizitolera msanga msonkho wa mafuta a galimoto kusiyana ndi kale.

President Lazarus Chakwera dzulo walandira sitimayi yomwe malinga ndi mkulu wa bungwe la NOCMA, a Clement Kanyama, yabweretsa mafuta okwana ma lita 1.2 million.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *