Phale wasagalatsa anthu adela leke powatengela kunyumba ya malamulo
Phungu wanyumba ya malamulo mdera la Salima north wati anthu a mdera lake adzidziwa zimene zimachitika mnyumba yamalamulo.
Phale wanena izi lero pa 3 September 2024 pamene akuluakulu achipani a mdera lake anabwera kunyumba yamalamulo.
Mmodzi mwa atsogoleri amene anabwera kunyumbayi, kamtolo kausiwa wati ndiosangalara kwambiri kuti wadziwa mmene aphungu aku nyumba yamalamulo amapangira zokambirana zawo.
” Ndasangalara kufika koyamba kunyumba ya malamulo, ndipo ndapeza kuti aphunguwa amakondana”, anatero kausiwa.
Nthawi zambiri anthu omwe amayika adindo mu mipando ngati aphungu saziwa zomwe zimachitika Kunyumba ya malamulo aphungu akamakumana.