Ndasiya kuyimba, watero Dan Lu
Mmodzi mwa akatswiri pa nkhani za maimbidwe mdziko muno Daniel Lufani yemwe amadziwika bwino ndi dzina loti Dan Lu wati wasiya kuyimba nyimbo.
Iye wanena izi pa tsamba lake la mchezo la Facebook kuti wasiya kuyimbaku chifukwa chakuti anthu asiya kukonda nyimbo zake zomwe zili mu mchimbale chomwe watulutsa kumene chomwe akuti “Back to my roots”.
“Ndasiya kuimba! Inu
Zoona mukusiya album ya nzeru ngati imeneyi nkumakapopa ma Bubblegum”
Dan Lu wapitiliza kunena kuti Pali anthu ena amene omwe akumuchitira kaduka kuti athane naye ndipo anthuwa apanga kale chithu chothekera kuti iye asamayitanidwenso ku mapwando amayimbidwe mdziko muno.
“Kuchita kupanga ma group special ofuna kuthana nane, ati osazampushaso, asamaitanidweso ku ma show, tizilemba nkhaniyake pokhapokha akapala kuti dzina lake likwililike ana ake siife!”.
Iye wadzudzulanso nkhalidwe la anthu ena amane amafuna kuti apatsidwe ndalama ndicholinga chakuti nyimbo za oyimba zipita patali.
Iye wati nkhalidwe limeneli ndi lomwe likupitsa pansi luso la mayimbidwe mdziko muno chifukwa oyimba ambiri sakupeza mphindu mumkuyimba kwawo.
Chimbale chomwe watulutsa pa 1 August 2024 Cha “Back to my roots” ndipo chili ndi nyimbo nkhumi (10) ndichomwe chautsa mapiri pachigwa pomwe zikuwonetsa kuti anthu sanachikonde.