Zatukusila ku Chipani Cha Kongelesi, Chipani chaluza mulandu
Chipani cha Malawi Congress Party chaluza mlandu okhudza kuika lamulo loletsa anthu ena achipanichi kuti asapikisane nawo pa msonkhano wake waukulu ngati sanakhale ma membala achipanichi kwa zaka ziwiri.
Malingana ndi chigamulo chomwe High Court Judge Howard Pemba wapeleka wati mamembala a chipanichi ndi omwe ali ndi mphamvu yosankha munthu yemwe akufuna osati komiti yaikulu kuchita chiganizo.
Zatelemu anthu onse omwe anawasiya kuti asapikisane nawo pa chisankhochi apikisana, izi kuphatikulizapo a Engineer Vitumbiko Mumba omwe akufuna kupikisana nawo pa mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleli wa chipanichi.