2025-02-19

Phungu apempha anthu kukalembasa mu Kawundula wa dziko

0
FB_IMG_1722111358249

Phungu wadera la kumwera kwa boma la Mulanje Santigo Phiri walimbikitsa anthu kudera lake kulembetsa mukaundula wa umzika ndikukhala ndi chiphaso kuti azathe kuzaponya nawo voti pa zisankho za m’chaka cham’mawa.

A Phiri anena izi loweruka pa msonkhano wachitukuko omwe achititsa dera la mfumu Makaula, mfumu yayikulu Mabuka m’bomalo komwe amatsegulira chitukuko cha mlatho komanso madzi a mpopi.

Iwo alimbikitsanso anthu akuderalo kukhala ndi umwini posamalira zitukuko.

Polankhulapo, mfumu Makaula yayamikira a Phiri kamba ka zitukuko zomwe akubweretsa kuderalo, ponena kuti zikuthandizira kupititsa patsogolo umoyo wa anthu m’magawo osiyanasiyana.

Pamwambowu panalinso masewero ampira wamiyendo pakati pa matimu a Black Eagles ndi Sanzikani FC pomwe timu ya Sanzikani yagonjetsa timu ya Black Eagles ndi chigoli chimodzi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *