“Ndine wokhutira ndimene amenyera anyamata anga” – Kamwendo

Wolemba Hosea Banda….
Yemwe akugwirizira ngati mphunzitsi watimu ya Creck Sporting, Joseph Kamwendo wati ndi wokhutira ndimene akumenyera mpira anyamata ake.
Kamwendo walankhula izi kutsatira kufanana mphamvu kwa timu ya Creck Sporting ndi Kamuzu Barracks pogoletsana zigoli ziwiri kwa ziwiri mu masewero a ligi ya TNM omwe anali pabwalo Aubrey Dimba boma la mchinji.
Iye wati panalibe yemwe amapereka mwayi kwa timuyi kuti ingakhale nawo mu gulu la matimu nkhumi omwe akuchita bwino mu gawo loyamba la ligi ya TNM.
“Ndine okhutila polingalira kuti panalibe yemwe amatipatsa mwayi kuti tingakhala nawo mumatimu nkhumi ochita bwino chifukwa timu ya Creck Sporting yangolowa kumene mu ligi ya TNM.”
Kamwendo wawonjezera kunena kuti anyamata ake asamataye mtima msanga pomwe amatsongola ndipo wati izi akazikoza pomwe akhale akukakumana ndi timu ya Premiere Bet Dedza Dynamos lolemba likudzali.
Ndipo mawu ake mphunzitsi wa Kamuzu Barracks, Charles Kamanga wati ndi zodandaulitsa poti timu yake yataya mapoinsi omwe amafunikira kwambiri kutimuyi.
“Ndizodandaulitsa kuti ngati Kamuzu Barracks tataya mapoitsi omwe amafunikira kwambiri kutimu yathu polingalira kuti timamenyera pankhomo pathu.”
Zeliat Nkhoma ndi Hope Mamadzunda ndiwo anagoletsera timu ya Kamuzu Barracks pomwe Frank Phiri ndi Anold Kiyama anagoletsera Creck Sporting.
Timu ya Creck Sporting ili pa nambala ya Chisanu mchiwiri (7) ndi ma poinsi 20 ndipo Kamuzu Barracks ili panambala ya chinayi ndi mapoinsi 23.
Mu masewero ena timu ya Civil Service United yafafana mphamvu ndi Mighty Tigers posagoletsana chigoli chilichonse pomwe timu ya Moyale Barracks inachita kuchokera kumbuyo kuti ifanane mphamvu ndi timu ya Bangwe All stars.