Musafooke, tiyeni mutitsatirebe kuti tichite bwino
Wolemba: Hosea Banda
Wachiwiri kwa mphunzitsi wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets Heston Munthali wapepha onse otsatira timu ya FCB Nyasa Big Bullets kuti apitire kuyitsatira timuyi posatengera kusachita bwino kwa timuyi.
Munthali wavomereza kuti timu ya FCB Nyasa Big Bullets sikuchita bwino ndipo izi sisachititse otsatira timuyi kuti abwerere m’buyo ndikusiya kutsatira timuyi.
“Tikupepha masapota nawo kuti atengepo mbali kuti ife aphunzitsi komanso wosewera tikhazikike ndipo atitsatirebe kuti tiwone kuti tikhazikika motani.” Watero Munthali.
Mphunzitsiyu amala khula izi kutsatira kungonja kwa timuyi ndi timu ya Karonga United ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi.
Babatunde aAdepuju adatsongoza timu ya FCB Nyasa Big Bullets mu phindi 28 muchigawo choyamba koma Saulos Moyo anabweza mu mphindi zitatu zowonjezera muchigawo choyamba chomwecho asanabwere Blessings Mwalilono ndi chigoli chopambanira mu phindi 68 muchigawo chachiwiri.
Zateromu timu ya FCB Nyasa Big Bullets ili pa nambala ya Chisanu ndi ma poitsi makumi awiri (20).