2024-10-04

Mphande wapempha achinyamata kuti asamakonde zithu zauler

0

Pemphero Mphande yemwe amathandiza anthu pankhani zosiyanasiyana, walimbikitsa anthu kuti asamakonde zinthu za ulele chifukwa sizingathe kuwapititsa patali.

Iye watinso anthu akuda azikondana pothandizana mukuchita zinthu za phindu zomwe zingathandize Dera lawo

Iye ana pereka chitsanzo Cha William Kamkwamba yemwe adapangako magetsi koma palibe munthu wa chikuda yemwe adabwera poyera ndi kumuthandiza.

Polankhula pomwe amaphunzitsa anthu pa momwe angapititsire patsogolo malonda awo, komanso mabungwe omwe amayrndetsa, mu mzinda wa Lilongwe, iye wati kupempha ndalama zongodyera ndikopanda phindu, kusiyana ndikuti anthu azipempha ndalama zoti ziwa pindulire.

Ndipo iye walimbikitsa anthu kuti azikondana ndikulimbikitsana pochita zinthu, ndicholinga Choti dziko lipite patsogolo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *