Mutharika Achezera Asilamu pa Mzikiti wa Mangochi
Wolemba: Emmanuel Matewere……..
Mtsogoleri wakale wa dziko lino yemwenso ndi Mtsogoleri wa Chipani cha Democratic Progressive Party-DPP, Professor Arthur Peter Mutharika anakachezera anzathu achipembezo Cha chisilamu pa Mzikiti wawukulu wa Mangochi.
Mwachizowezi, a Mutharika anachezera komanso kuwalimbikisa abale ndi alongo achisilamu amene padakali pano ali mu nyengo ya Ramadan. Iwo ananena kuti nyenyo ya Ramadan ndi yofunikira kwambiri imene ili nthawi imene otsatira chipembezo Cha chisilamu amayandikana ndi Mulungu (Allah) posala kudya, komanso kuchita ntchito zachifundo (Zakaati).
Pofuna kuwonetsa chikondi chawo, A Mutharika agawa zakudya monga mpunga, sugar komanso ufa zoti anthu pa mzikitipa azigwiritsa ntchito amakamasula Ramadan.
Paulendowu, Iwo anaperekezedwa ndi Olemekezeka Sameer Suleman MP, olemekezeka a Ralph Jooma, Sheik Salire Saidi komanso akulu akulu a chisilamu m’bomali.
Poyankhulapo, mmodzi mwa akuluakulu a chipembedzo cha chisilamu womwe anali nawo pa mwambowu anati Professor Mutharika wakhala akuchita izi chaka ndi chaka ndipo asilamu wonse ku Mangochi ndiwokondwa chifukwa akawona Professor Mutharika akuwayendera amalimbikitsika ngakhale akudutsa mmavuto osiyanasiyana.
A Mutharika womwe ali ndi achibale ambiri omwe Ali achipembedzo cha chisilamu afunira asilamu wonse mdziko muno pamene ali munyengo imeneyi ya Ramadani