Chipani cha LEF chaunikira anthu mfundo zake mozama
M’tsogoleri wa chipani cha Liberation for Freedom Party(LEF),David Mbewe PhD ,waunikira anthu za zina mwa mfundo zake pofuna kuti azimvetse mozama pomwe chisankho cha pa tati cha 2025 chayandikira.
“Tikamati Malawi wa chuma, wokhalika, wa mtendere mwa zina, tikutathauza chani?” anafunsa motero mtsogoleriyu.
Mbewe anati ili litha Kukhala limodzi mwa mafunso omwe anthu m’dziko muno alinawo.
Iye watinso m’malo mwa chipani chonse cha LEF adzapanga dongosolo lophunzitsa anthu kukhala odzidalira pawokha osati kudzawagawira ndalama.
“Munthu mukamupatsa Nsomba akadya ikatha abwera kudzapemphanso ina,koma mukamupatsa mbedza apa apita akawedza ina paiye yekha ndikudya,choncho ndi upangiliwu anthu adzidzazidalira pawokha” watero Mbewe PhD,M’tsogoleri wa Chipani cha LEF.poyakhula kudzera pa tsamba lake la m’chezo la Facebook patsindika pa godya zake monga MalawiWachuma, Wokhalika, Wamtendere.