2024-06-14

Namondwe atha kubuka pa nyanja ya mchere, yatero nthambi ya za nyengo

0

Wolemba Hosea Banda……

Nthambi yowona za kusintha Kwa za nyengo mdziko muno yatulutsa chikalata chochenjeza a Malawi kuti kutha kubuka namondwe pa nyanja ya mchere ya India.

Nthambiyi yati namodweyi panakali pano sanabandwe ndipo Pali chiyembekezo chakuti atha kubadwa pofika lamulungu likudzali pa March10,2024.

Ndipo yawonjezera kuti nthawi yomwe namondweyi adzatenge kuti achepe mphamvu yake sikudziwika.

“Chifukwa chakuti namondweyi sanabadwe sizikudziwika kuti azatenga nthawi yayitali bwanji kuti adzachepe mphamvu.”

Chikalata chomwe nthambiyi yatulutsa chaonjezera kuchenjeza anthu onse mdziko muno kuti apewe kuwoloka mitsinje yodzadza powopa ngozi.

Izi zadza pomwe nthambiyi yachenjezanso anthu okhala chigawo Cha kumpoto Kwa dziko lino komanso onse okhala mu maboma a phepete mwa nyanja kuti palinso chiopsezo Cha kusefukila Kwa madzi komwe kudze kamba ka mvula ya mphamvu yomwe igwe kuyambira pa March 7,2024.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *