2025-03-18

Maganizo: Amangoyenela Kunjatidwa Anatasa Kwambiri Billy Malata

0
FB_IMG_1705316114838

By Nicolette Nsimtama……..

Nkhani ili mkamwakamwa ndi ya Fredrick Billy Malata munthu amene anaonetsa khalidwe lonunkha loyipitsitsa lomwe aliyense anadana nalo.

Zomwe Billy Malata wakhala akuchita zinachoka pa ndale ndikufika pa ma personal attacks. Billy Malata wakhala akutukwana komanso kunyoza aliyense wa chipani cha DPP posayang’ana udindo wa munthu.

Malata chomwe amadziwa ndi kutukwana atsogoleri, kuwaopseza kuti awayalutsa popeka nkhani zosiyanasiyana zabodza zomwe zimakhala zofuna kuononga mbiri ya chipani cha DPP.

Ma uthenga amene takhala tikuwerenga pa masamba a michezo monga pa Facebook komanso WhatsaApp amaonetseratu poyera kuti Billy Malata amagwiritsa ntchito kuononga mbiri ya ena ndikuwaopseza kuti apeze khobidi.

Ena mwa anthu amene akumudziwa Malata anatsimikiza. Kuti izi ndi zoona ndipo asanalowe chipani cha DPP iwo amachitanso khalidwe loyipitsitsali ku chipani cha PP ndipo anauzidwanso kuti akasumiridwa.

Ku MCP Billy Malata anayambanso khalidwe lomweli atangolandila chikalata cho chotsedwa mu chipani cha DPP mission yake yonse inafoyira ndipo anthu anamuona kuti ndi munthu osafunikila ndipo anamukanthako.

Lero sizodabwitsa kumva kuti Billy Malata wamangidwa izi ndi zimene anthu ambiri amayembekezera ndipo amafunitsitsa zikadachitika poyambililira. Amalawi afuna chipani cha DPP chilowenso m’boma ndipo munthu osokoneza ngati Malata siwoyenela kumusunga.

Ulemu upite kwa akulu akulu onse achipani Cha DPP posalora kuti wina wa mutu wa namtongwe adetse mbiri zawo. Ndipo ena nonse amene mwatchulidwa maina mu nkhani ya Malata tenganipo gawo mosanyengerera. Malata awone chinameta nkhanga mpala.

Akulu akulu amene anatchulidwa maina mu zolemba za Malata ndi anthu odziwika ndi mbiri zabwino pa Malawi pano ndiponso ndi amene ali ndi udindo mu society, business sector, politics , religion ndi m’malo ena choncho kuwaonongela mbiri chonchija inali mistake yayikulu akungoyenela kulandila chilango chokhwima kuti achimine.

Aliyense amene akuyikila kumbuyo Billy Malata ameneyo tiyeni timudabwe ndekuti amadya naye limodzi ndalama zimene amazipeza mu njira yolakwikayi.

 

CHIZIWITSO:….

Dziwani kuti zonse zomwe zalembedwa mu nkhani iyi si maganizo a “The Malawi Guardian” koma a mwini walemba nkhaniyi

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *