Kuchepa Kwa ukhondo Misika Kukupeleka Chiopsezo Chamatenda

Wolemba: Hosea Banda……….
Anthu okhala pafupi pa msika wa pondamali Ali pa chiopsezo chodwala matenda osiyanasiyana kamba ka dzala lomwe liri Malo okhalako anthu.
Kafukufuku wa Malawi Guardian online wapeza kuti msika wina odziwika kuti Pondamali omwe uli m’boma la LILONGWE ukutaya zinyalala Malo omwe kuli nyumba za anthu zomwe zikupereka chiopsezo Cha matenda osiyanasiyana omwe amadza kamba kosoweka ka okhondo.
Malawi Guardian online itayendera malowa inapeza kuti pamalowa palinso zimbudzi zomwe zimagwiritsidwa ntchito pamsikawu komanso Pali nyumba zomwe anthu amakhalamo ndiso kuti pamalopa pakumveka fungo losakhala bwino.
China chomwe The Malawi Guardian online yapeza kuchokera pamalowa ndichakuti Ndi imodzi mwa njira yolowa mkati mwa nsikawu.
Ndipo malipoti ena akusonyeza kuti munthu mmodzi anafa Ndi matenda a kolera mderali, ndiso kuti nyumba ya munthu yemwe anafa Ndi matendawa ili pafupi zedi ndi dzala la msikawu.
Boma la Lilongwe ndi boma limodzi lomwe lankhudzidwa kwambiri Ndi matenda otsekula mimba a kolera omwe apha anthu ochuluka bomali.