2024-06-13

FAM Yatsutsa Phekesela za masewera a Egypt achibwereza kuti adzaseweredwa Usiku

1

By Vitumbiko Mvula……..

Bungwe limene limayendetsa masewero a mpira wa miyendo mdziko muno la Football Association of Malawi (FAM) latsutsa mphekesera zoti masewero achibwereza a pakati pa ma team a Malawi ndi Egypt adzaseweredwa usiku.

Mkulu oona za malonda ku bungweli, Limbani “Cliff” Matola amene akufalitsa bodzali akuyenera kulapa kwa Mulungu.

“Amene anayambitsa bodzali akuyenera Kuti alape kwa Mulungu kupempha chikhululukiro ponena bodza ,masewero azayamba 3:00 masana,” watero Matola.

Team ya Malawi ili m’dziko la Egypt kumene ikhale ikukumana ndi ana a Pharaoh madzulo ano nthawi ya 9 koloko mmasewero olimbirana malo ku mpikisano wa ma team a mu Africa wa chaka cha 2023 kapena kuti 2023 TotalEnergies African Cup Of Nations.

Pamene Malawi ikhale ikufunafuna chipambano chawo choyamba ku Egypt, Matola wati zokonzekera zonse zili bwino ndi Flames ndipo wapempha a Malawi Kuti ayifunire zabwino ndikuyipempherera Flames.

“Osewera athu alikuthekera kosewera usiku chifukwa sikoyamba kusewera usiku kotero Ali ndi ukadaulo wabwino
ndithu,” anaonjera motero Matola.

Mphunzitsi wamkulu wa team-yi, Mario Marian Marinica wati anyamata ake ndi okonzeka kuchita zinthu ku Egypt chifukwa m’chipululu simofera.

Malawi ili pa nambala yachiwiri pa ndandanda wa ma team anayi mu Gulu D limene ma team onse ali ndi ma poinsi atatu koma zigoli zochinya ndi zochinyitsa ndi zimene zikusiyana.

Pamene Malawi ikhale ikupalana mamba ndi Egypt, Ethiopia ndi Guinea nawonso akhala ali m’bwalo.

Follow Us on Twitter: @GuardianMalawi1

1 thought on “FAM Yatsutsa Phekesela za masewera a Egypt achibwereza kuti adzaseweredwa Usiku

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *