Flames ilibe chisankho koma kupambana – Chinyama

0

By Vitumbiko Mvula……….

Katswiri pa Nkhani zamasewero mdziko muno Parry Chinyama wati timu ya mpira wamiyendo ya dziko lino The Flames ilibe chisankho Koma kupambana pamasewero ake mawa.

Chinyama wanena izi posatira zomwe ananena mphunzitsi wankulu watimuyi, Mario Marinica kuti timuyi itha kulephera kuchita bwino pamasewero ake mawa kamba koti aseweredwa usiku pomwe osewera athu sanazolowere. Marinica watinso sakuyembekezera mayere aliwonse kuchokera Kwa osewera akunja kamba koti anali ndinthawi yochepa kukozekera masewerowa.

Poyankhula ndi The Malawi Guardian Chinyama wati Marinica wanena izi Kuti apeze pothawira chabe mtsogolo muno ,kusewera usiku chisakhale chifukwa chogonjera kamba koti timuyi inasewerako usiku Ku FIFA ndikuchinya timu ya Zimbabwe .

“Mphunzitsi wa timuyi amaziwa ndipo pokonzekera masewero mawa amayenera kukonzekera usiku “

Iye anawonjezera kunena Kuti Ngati timuyi igonje mawa tiyembekezere kuzasamba zigole pakhomo zomwe zizakhale zochitisa manyazi.

Timu ya Flames idalonjedza chipambana pamasewero ake pofuna kupereka ulemu wawo kwa a Malawi ambiri omwe ataya miyoyo yao pa Namondwe ya Freddy amene wakhudza kwambiri chigawo chakumwera mudziko muno.

Timu ya dziko lino The Flames ikhale ikukumana ndi ana a Farao mdzinda wa Cairo mawa 8:00 madzulo ndipo pa 28 mwezi uno ,matimuwa akumanenso pa Bingu International stadium mdzinda wa Lilongwe.

Timu ya Egypt ili pa nambala 39 pamundanda wa matimu Ku AFCON ndipo ndi timu yomwe ikuoneka ya bwino Kuno Ku Africa.

Follow Us on Twitter: @GuardianMalawi1

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *