Bungwe la APAM Lati nalo ndilokhuzidwa ndi ngozi ya Cyclone Freddy

Wolemba: Hosea Banda……..
Pomwe anthu akufuna kwabwino komanso mayiko akupitilira kutumiza thandizo Kwa anthu omwe ankhudzidwa Ndi namondwe wa Freddy yemwe wakhudza Kwambiri maboma achigawo Cha kumwera Kwa dziko la Malawi, bungwe la anthu omwe ali Ndi khungu la achi albino la Associations of People Living with Albinism in Malawi (APAM) lati nalo lakhudzika Kwambiri Ndi namondweyi.
Polankhula Ndi The Malawi Guardian online mtsongoleri wa APAM Young Muhamba wati anthu opusa makumi asanu ndi limodzi (66) achi albino ndiwo akhudzika Ndi namondweyi ndipo athawa nyumba zawo zawo.
Iye wati Boma la Phalombe Ndi lomwe likuonetsa chiwerengero chochuluka Cha anthu achi albino omwe athawa nyumba zawo ndipo akukhala misasa yomwe yakozedwa.
Malingana ndi a Muhamba ati anthu pafupifupi makumi asanu (50) achi albino ndiwo akhudzika Ndi namodweyu pomwe nyumba Ndi katundu wawo wawonongeka Ndi namodwe wa Freddy. Iye anapitilira kunena kuti chiwerengerochi chitha kukwera potengera kuti sanamalize kafukufuku wawo.
Muhamba wati bungwe lawo likuyesetsa kuti lifikile maboma onse ndukudziwa chiwerengero Cha anthu achi albino omwe akhudzika ndi namondwe wa Freddy. Iye watinso akudziwa kuti anthu akhungu la achi albino amafunikila mafuta oti azidzola, ndipo mafuta a anthu ambiri akhungu la achi albino mafuta awo akokoloka kudzatira kudza Kwa namodweyu ndipo wati anthuwa akufunika kuti apite muzipatala ndikukatenga mafuta ena.
Mtsongoleriyu wapepha onse akufuna kwabwino kuti athandize Ndi kuganizira anthu onse a ulumali omwe akhudzika ndi namondwe wa Freddy yemwe wakhudza Kwambiri maboma achigawo Cha kumwera Kwa dziko la Malawi.
Bungwe la Association of People Living with Albinism in Malawi (APAM) limayembekezereka kuchita ziwonetsero zowonetsa kusakondwa ndi ndondomeko ya zachuma ya Chaka Cha 2023 mpaka 2024 ponena kuti nfondomekoyi yasala anthu achi albino mdziko muno. Ndipo Iwo ati ayimitsa Kaye zionetserozi mpaka mtsongolomu polingalira kuti dziko lino liri pamavuto a namondwe wa Freddy.
Follow Us on Twitter: @Guardian_Malawi1