Kuchepasa mphamvu za mtsogoleli wa dziko nkwabwino – Watelo Kondowe

0

Wolemba: Hosea Banda…….

Wolankhulapo pa nkhani za ulamuliro wabwino mdziko muno Ceaser Kondowe wati ganizo la aphungu otsutsa Boma mnyumba ya malamulo lofuna kubweretsa bilu yofuna kuchepetsa mphamvu za mtsongoleri wadziko Ndi labwino chifukwa lipangitsa kuti katangale achepe mdziko muno.

Iye wati ganizo lobweretsa biluyi lithandizira kuti nthambi zambiri za Boma ziyambe kugwira ntchito zake momasuka ngati biluyi ingadutse ndikukhala lamulo mdziko muno.

Izi zikudza pomwe mtsongoleri wa mbali yotsutsa Boma mnyumba ya malamulo Kondwani Nankhumwa wati mphungu wina wambali yotsutsa Boma akufuna kubweretsa biluyi kunyumba ya malamulo kuti aphungu a nyumbayi adzakambilane kuti likhale lamulo.

Kondowe wati mtsongoleri wadziko lino Dr Lazarous Mac Cathy Chakwera amakhala akuyankhula munyengo yokopa anthu kuti adzamuvotere kuti iye akadzalowa Boma adzachepetsa mphamvu zomwe zimakhala Ndi mtsongoleri wadziko lino.

Lachiwiri lapitali pa 28 February 2023, aphungu a nyumba ya malamulo anafunsa mtsongoleri wadziko lino Dr Lazarous Mac Cathy Chakwera kuti chifukwa chiyani sakuchepetsa mphamvu za mtsongoleri wa dziko lino ndipo Mtsongoleriyu poyankhapo anati Ndi udindo wa nyumba ya malamulo komanso nthambi zoona Ndi kukoza malamulo mdziko muno kuti zipange zothekera kuti mphamvu za mtsongoleri wadziko lino zichepe.

Ceaser Kondowe anawonjezera kuti ngati biluyi ingabwere kunyumba ya malamulo ndikukanidwa ndiye kuti zidzaonetseratu kuti anapanga chibisalira ndipo anati ngati biluyi idzadutse ndiye kuti mtsongoleri wadziko Lina amanena zoona.

Ngati biluyi ingaditse ndikusandika lamulo ndiye kuti mtsongoleri wadziko lino sadzakhalanso Ndi mphamvu zosankha mkulu wa bungwe lothana ndikatangale la Anti-Corruption Bureau (ACB) ndiso kupereka umwayi oti mtsongoleri wadziko atha kuzengedwa Ndi kuyankha milandu Ali paudindo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *