2025-03-19

Timu ya Marine yati yikufunabe kusewela mu ligi yayikulu

0
IMG-20230221-WA0052

Wolemba: Hosea Banda……..

Timu ya asilikali ankhondo ya madzi yochokera Boma la mangochi ya MDF Marine yati loto lawo lofuna kusewera mu ligi ya TNM linakalipo ndipo aonetsetsa kuti Chaka chino achilimike Ndi kulowa mu ligiyi.

Mlembi wamkulu wa timu ya MDF Marine yomwe imasewera mu ligi ya chigawo chakumwera ya southern Region Thumbs up premier Division Staff Sargent Frank Maudzu wati Ndi khumbo lawo kuti timu ya MDF Marine ilowe mu ligi ya TNM sizoni ikubwerayi ya 2023.

“Ku nkhani yokozekera sitinayambe Koma tikhala tikuyamba pompano ndipo ndili Ndi chidzimikizo kuti sizoni inoyi ulendo ukalowa mu TNM super league ulipo”.

Maudzu wati timu yawo inali Ndi mvuto la omwetsa zigoli lomwe linakhudza kwambiri kaseweredwe ka timuyi ndipo Ndi chimodzi mwa zithu zomwe zapangitsa kuti timuyi imalizire pa nbala yachitatu mu ligi ya ku mwera ya Thumbs up. Iwo anawonjezera kunena kuti kumbali yawo anayesetsabe kuchilimika kuti timuyi iyambe kuchita bwino ndikutenga ukatswiri wa ligi ya chigawo chakumwera Koma izi sizinatheke.

Timu ya Nyasa Big Bullets Reserve ndiyomwe inakhala akatswiri a ligi ya kumwera ndipo timu ya Bangwe All Stars inakhala pachiwiri pomwe MDF Marine inamaliza pachitatu mu ligiyi.

By: Hosea Banda

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *