Mkumano wa Mayamiko Stars unali wothandiza
Wolemba Suzana Nkhoma……..
Potsatira chiganizo chothetsa ma udindo onse, timu ya Mayamiko Stars, amenenso Ali akatswiri a mpikisano wa Nyasa capital finance cup mchigawo Cha kumpoto anakonza nkumano omwe cholinga chake chinali kufuna kudziwa athu omwe angafune kuzapikisana nawo pa zisankho zofuna kupeza ma udindo atsopano.
Ena mwa omwe anapezeka ku nkumanowu ndi Mkulu oyang’anila timuyi a Mayamiko Tembo omwe anafotokoza kuti cholinga chenicheni Cha nkumanowu chinali chofuna kumva nzeru za anthu osiyanasiyana malingana ndi momwe angapitisile timuyi patsogolo.
“Tikufuna anthu omwe angathe kuithandizira timuyi kupita chitsogolo, ichite bwino kuposa mmene inapangira Chaka chatha, A Tembo adafotokoza”.
A Tembo atinso anthu omwe akuona kuti Ali ndi kuthekera kokhala mma udindo amenewa asaope kutumiza mfundo zawo pasanafike pa 20 February 2023.
Mmodzi mwa omwe asankha kupikisana nawo pa zisankho zi a Afiki Brown ati Iwo Ndi okonzeka kuthandizila timuyi kuti idzalowe nawo mu mpikisano wa TNM superleague.
Zisankho zizachitika pa 26 February 2023.