2024-11-02

Ndende ya Mzuzu ikhazikisa kalabu ya nkhonya

0

By Susan Nkhoma:…….

Kunali Mvula ya zibagela pa Mzuzu prison komwe kunali masewera a Nkhonya otchedwa Youth Open Boxing challenge pa tsiku loweluka masana.

Masewelawa inali njira imodzi yokhazikitsila kalabu ya Nkhonya yotchedwa Mzuzu Prison boxing club.

Masewerawa anatulutsa anyamata achisodzera, Ishmael Zamba komanso Gerald Kabichi omwe anafananitsa Mphamvu ataonetsana zigogodo zankhani nkhani.

Poyankhula atatha masewerawa Mkulu waboma wiyang’anila masewelo mu chigawo Cha ku mpoto a Gracian Mkandawire wati kubadwa Kwa Boxing club ngati Imeneyi pa Mzuzu prison kuthandiza amalawi munjira zambili makamaka kumbali ya achinyamata a mzinda wa Mzuzu omwe azikhala ndi chidwi ndi Masewero ngati amenewa mmalo mopanga Zina zosayenera.

Poonjezera apo oyankhulira mbali ya omwe akuthandizila Masewero amenewa Austin Shaba ati Iwo cholinga chawo chofuna kupititsa masewerowa pamwamba makamaka mu mzinda wa Mzuzu chitha kukwanilitsidwa Poona kuti anthu ambili akuonesa chidwi pamasewero amenewa. A Shaba atinso komiti yawo yakonzanso ndondomeko yoti imeme atsikana komanso amai kutenga nawo mbali pamasewerowa mu mzinda wa Mzuzu.

Iwo atinso komiti yawo yomwe ikutsogoleledwa ndi a Victory Nyirenda kuyembekeza kuthandizila Masewerowa Mmalo ena ndi ena Malawi muno.

Mlembi wamkulu ku chigawo Cha ku mpoto ku bungee ka Maba a Mike Lyson Zgambo ati ndiwokondwa chifukwa zipaso za kubwera kwa ling’i zayamba kuwonela ndipo Iwo ati masewelowa ndi mbali imodzi yothandiza kupeza anyamata omwe atakayimile anzawo ku masewero omwe atachitike mu disembala Chaka chino.

Awa anali masewelo achiwiri pansi pa bungwe la MABA muchigawo chakumpoto kupangika.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *