2024-11-04

Osewera Mpira wa miyendo a Malawi amwemwetera ndi Basi yatsopano

0

Amene anatsogolera wosewera azake pa mwambo wolandira Basi kuchokera ku banki ya FDH kupita ku timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino Stanley Sanudi wati basi yomwe alandira ipeleka mangolemera kwa osewera a timu ya dziko lino kuti ayambe kuchita bwino mu mipikisano yomwe ikubwera kutsogoloku.

Sanudi wayankhula izi pa mwambo womwe unachitira ku likulu la Bankiyi mu mzinda wa Blantyre ndipo wati chimodzi mwa zinthu zomwe achite ngati wosewera ndi kuchita bwino komaso kudzipezera malo mu ndime yotsiliza ya mpikisano wa AFCON.

Malinga ndi Sanudi amene nthawi zina amatsogolera timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino m’bwalo la zamaseweo wati ndi zosangalatsa kuti banki ya FDH ikupitiliza kukhala bwezi losawona nyengo ku timuyi.

“Ndife wokwendera kwambiri ndi zomwe a banki ya FDH atichira potigulira basi yamakono ngati yimeneyi ndipo zitithandiza kutipatsa chilimbikitso pa masewero anthu ngati wosewera a timu ya dziko lino,” Sanudi anatero

Komabe katswiriyu amene amasewera ku manja cha kumbuyo kwa timu ya Mighty Mukuru Wanderers anawonjezera kuti zomwe zachitikizi zipangitsa kuti adzalimbikire pa masewero ofuna kudzigulira malo mu ndime yotsiliza ya mpikisano wa AFCON.

Malinga ndi Antondo womwe omukonda ambiri amanenera wati anthu dziko muno ayembekezere timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino yosinthika pakaseweledwe kake ndipo wosewera wina aliyese ndiwokozeka kuwonetsa chithokozo chake ku banki ya FDH kudzera mkuchita bwino pa masewero atsogolomu.

“Chimodzi mwa zinthu zomwe tichite ngati wosewera ndikulimbikira kwambiri mpakana titachita bwino mu mpikisano wa AFCON ndipo zimenezi tiyambira pa masewero womwe tidzakhale nawo ndi timu ya Egypt kumayambiliro kwa chaka cha mawa,” Anafotokoza motero Sanudi.

Aka sikoyamba kuti banki ya FDH ikhale ikuthandiza pa nkhani za masewero dziko muno pomwe mbuyomu yakhalaso ikupeka ndalama ku timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino.

Kupatula kuthandiza timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino, banki ya FDH imapelekaso ndalama za nkhani nkhani mu mchikho cha FDH chomwe wopambana amatenga ndalama zokwana 25 million kwacha.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *