Silver yayika maso ake pa chikho cha Airtel Top 8
……..Komanso kusiliza ligi pa mundandanda wa ma timu anayi……
Wolemba Lucky Millias:….
Akulu akulu womwe amathandiza timu ya Silver Strikers apeleka mulingo kwa aphudzitsi womwe angosankhidwa kumene kuti atenge chikho cha Airtel Top 8 kulephera apo ntchito yawo idzakhala pa chiopsezo.
Mlembi wa kampani yomwe imathandiza timuyi a Peter Masiye ayankhula izi patangodutsa masiku ochepa timuyi italengeza kubwera kwa m’phudzitsi watsopano Edison Kadenge Mwafulirwa kuti akhale wachiwiri wa mphudzitsi wa timuyi kulowa m’malo mwa Mcdonald Yobe amene watsitsidwa pa udindo wake ndikuuzidwa kuti azikaphudzitsa timu Silver Strikers Reserve.
Masiye wati iwo ngati othandiza timuyi ndiwokozeka kuchita china chilichonse chofunikila kuti zinthu zisinthe ku dera la ku 47 mu mzinda wa Lilongwe komwe timuyi imachokera kuti chisangalaro chibwelereso.
“Zinthu zakhala zikukanika kusongola ku timu kwathu maka pa zotsatira zomwe timu yakhala ikupeza pa bwalo la za masewero mumipikisano yosiyanasiyana ndipo kusintha komwe kwachitikaku tili ndi chikhulupiliro kuti zotsatira zisinthaso,” Masiye anatero.
Masiye anapitiliza kuti chimodzi mwa zinthu zomwe akufuna kuti aphudzitsiwa achite ndikutenga chikho cha Airtel Top 8 ndipo kulephera apo ntchito yawo idzakhala pa mpeni.
Iwo anamvomeleza kuti ndi momwe mpikisano wa ligi ya TNM ukuyendera ndi zokayikitsa kuti timu yawo ingakwanitse kuphumitsa timu ya Nyasa Big Bullets yomwe ikutsogola ndi 55 poitsi itasewera masewero okwana 21 kotero chinthu cha mzeru chomwe angachite ndi kuyika maganizo awo onse pa chikho cha Airtel Top 8 chomwe chikhale chikubwera posachedwapa.
“Chomwe tasinthira maudindowa ndikufuna kuti timu isinthe kaseweledwe kake komaso atitengere chikho cha Airtel Top 8 kulephera apo ntchito yawo tidzayenera kuyiwunikilaso kumapeto kwa chaka cha zamaseweo ngati kuli kofunika kupitilira kukhala nawo kapena ai,” Masiye anatero.
Pakadali pano Masiye wapempha ochemelera a timuyi kuti apewe kuchita zinthu zobweretsa chisokonezo pomwe timuyi ikusewera masewero ake.
Koma mkuyankhula kwake mkulu wa ochemelera wa timuyi a Brandson Levison ati iwo akuyembekezera kusintha pakaseweledwe kamaso zotsatira za timuyi kutsatira kusintha komwe kwachitika pa ophudzitsa timuyi.
Levison anaonjezera kuti ndi zinthu zokhumudwitsa kuwona timu yomwe yakhala ikutenga zikho komaso ligi ikumvutika kupeza chipambano chokhazikika mu masewero osiyanasiyana.
“Ndigwilizane nawo a Masiye kuti chomwe chikufunika ndi chikho cha chikulu kuti chibwere ku timu kwathu ndipo ndi momwe zilili pakadali pano chikho chake ndi cha Airtel Top 8 basi.
“Ngati ochemelera tiwapatsa chilichonse chomwe aphudzitsiwa afune kuchokera ku mbali yathu ndipo tikufuna kusache opanda m’dipo,” Levison anatero.
Koma modzi mwa akatsiwri pa nkhani za masewero amane amakonda kuyankhula pa wailesi ya Kasungu Fm Vincent Chapuzga wati zinthu zikhoza kusintha ku timu ya Silver Strikers ngati aphudzitsi atsopanowa angayambe kukhulupilira osewera womwe ali ndi kuthekera kubweletsa chimwemwe kusiyana ndikumalowetsa osewera mwa chizolewezi.
“Timu ija ili ndi osewera abwino kwambiri koma mvuto ndiloti onsewera ena sapatsidwa mpata osewera pafupipafupi ndipo m’mwalo mwake amakakamira wosewera omwe nthawi yawo ili kumapeto ngati Blessings Tembo, Frank Banda, Tawonga Chimodzi kungotchulapo ochepa,” Iwo anatero.
Pansi pa kusintha kwa tsopano, timu ya Silver Strikers iziphudzitswidwa ndi Leo Mpulura pomwe mphudzitsi wakale wa Ekwendeni Hammers Edison Kadenge Mwafulirwa akhala wa chiwiri ndipo Peter M’gangira akhala othandiza wachitatu kuphudzitsa timuyi pomwe Victor Mphande ndi ophudzitsa otseka pagolo ndipo Young Chimodzi Jnr ndi oyang’anira osewera.
Silver Strikers ili pa nambala ya chisanu (5) pa ndandanda wa ma timu a mu ligi ya TNM ndi mapoitsi okwana 38 itasewera masewero okwana 23 ndipo idatuluka kale mu mchikho cha FDH Bank pomwe idagonja ndi timu ya Dedza Dynamos Salima Sugar kudzera pa mapenate.