Plan International Malawi ikhazikitsa chikho cha Mpira cha ndalama za nkhani nkhani ku Dowa

0

Olemba Lucky Millias

Akulu akulu oyendetsa masewero a mpira wa miyendo m’boma la Dowa mogwirizana ndi bungwe la Plan International Malawi akuyembekezera kukhazikitsa chikho cha ndalama zokwana 6 million mwezi uno.

Malinga ndi mlembi wa mkulu wa Dowa District Football Association Joseph Kamanga wati mpikisanowu ukhala pakati pa matimu ochokera mu m’sasa wa Dzaleka komaso ma timu ochokera m’boma la Dowa.

Kamanga anati cholinga cha mpikisanowu ndikufuna kuti pakhale kuchitira zinthu limodzi pakati pa mzika zomwe zikukhala mu msasawu ndi anthu okhala m’boma la Dowa.

“Tithokeze kuti a Plan International Malawi atiganizilaso zotipatsa mpikisanowu chaka chinoso. Ngati akulu akulu oyendetsa masewero kuno ku Dowa tiyesetsa kuti mpikisanowu tiwuyendetse bwino,” anatero Kamanga.

Komabe Kamanga anapitiliza kuti mpikisanowu ukhudzaso masewero ena monga masewero a mpira wa manja komaso masewero a mpira wa miyendo koma osewera ake ali atsikana.

Malinga ndi Kamanga wati mpikisanowu ukuembekezera kuyamba pa 17 mwezi uno lomwe ndi la chiweru likudzali pomwe ma timu a Mpalankhwali adzakumane ndi timu ya Nkhono pa bwalo la Dowa Community.

Ena mwa ma timu omwe akhale akutenga nawo gawo mu mpikisanowu ndi monga Dowa Hammers, Nyundo Even Sporting, Sweepers, City Star, Lirambwe komaso Dowa Young Academy.

Zina mwa zinthu zomwe matimuwa apindule kudzera ku mpikisanowu ndi monga mipila, zomvala zosewelera masewero komaso ndalama.

Aka sikakhala koyamba kuti bungwe la Plan International Malawi likhhazikitse chikho ngati ichi chifukwa chaka chatha mpikisano ngati uwu udachitikaso m’bomali.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *